Mopemphedwa ndi Unduwa wa Zaumoyo, nthambi yapadera yoona zamalamulo mudziko muno linaunika ndondomeko za malamulo ndi zilango zake zokhuzana ndikuchotsa pakati ndipo muchaka cha 2015 anabweretsa ganizo la lamulo lovomereza kuchotsa pathupi.
Zafotokozedwa pansipa ndi chidule cha lamulo lovomereza amayi kuchotsa pathupi monga m’mene linapagilidwa ndi nthambi yoona zamalamulo. Kufotokoza uku cholinga chake sikulowa m’malo mwa lamulo loyambilira lovomereza amayi kuchotsa pathupi komanso sikukuyenera kusokonezedwa ndi kumasulira kwina kulikonse komwe kulipo.
Mutu wachidule ndi matanthauzo (Gawo 1 ndi 2)
Gawo loyamba likufotokoza mutu wachidule wa lamulo limene lizadziwika ngati: Lamulo Lovomereza Kuchotsa Pathupi. Gawo limeneli likufotokozeranso kuyamba kugwira tchito kwa lamuloli.
Gawo lachiwiri likutanthauzila mawu ena omwe agwiritsidwa ntchito mulamuloli monga “opereka thandizo lazaumoyo ovomerezeka).
Zifukwa zololedwa pamene munthu wafuna kuchotsa pathupi (Gawo 3)
Lamulo lovomereza kuchotsa pakati lizalola munthu kuchotsa pakati pokhapokha ngati pachitika zinthu izi:
- Kupitiliza kulera pakatipo kukhoza kuyika moyo wa mayi pachiopsezo
- Kufuna kupewa kuvulala kwa pathupi komanso maganizo a mayi oyembekezera
- Pali kusintha kwakukulu kwa khanda losabadwalo mokuti silingathe kukhala moyo litati labadwa.
- Pathupipo pabwera kaamba kogwiriridwa kapena ndipopatsana pachibale.
Ngakhale izi zili chonchi, ndikofunika kutsindika kuti:
- Ngati pathupi pabwera kaamba kogwiriridwa kapena ndipopatsana pachibale, mzimayi akuyenera akhale kuti nkhaniyi anakayipereka ku polisi kuti akhale ovemerezeka kuchotsa pathupipo malingana ndi gawo lachitatu.
- Mavuto azachuma komanso zachikhalidwe sizizagwiritsidwa ntchito. Mwachitsanzo, mayi sazaloledwa kuchotsa pakati pachifukwa chokuti akufuna apitilize ndimaphunziro ake.
- Kuchotsa pakati sikuzaloledwa chifukwa mayi wafuna kuti kuchitike. M’malo mwake, ogwira ntchito zaumoyo, movomerezedwa ndi lamulo kuti achotse pathupipo, azaunguza ngati zifukwa zololedwa ndi lamulo kuti atha kuchotsa pakati zilipo.
Malo omwe kuchotsa pathupi kutha kuchitikila (Gawo 4)
· Kumalo okhawo ovomerezedwa ndi Unduna wa Zaumoyo ndi chilangizo chotsindikidwa mu nyuzipepala (Gazette)
· Povomereza malo, izi ndi zina za zomwe Nduna ya Zaumoyo izalingalire:
- Pathupi posaposera masabata 12 pakhoza kuchotsedwa kuchipatala chachin’gono kapena chipatala chachikulu
- Pathupi poposera masabata 12 kukhoza kuchotsedwa ku chipatala chachikulu basi
Ogwira ntchito zaumoyo amene akhoza kuchotsa pakati (Gawo 5)
· Pathupi posaposera masabata 12 kukhoza kuchotsedwa ndi wothandizira adokotala, namwino othandizira mzamba komanso namwino kapena mzamba ovomerezeka.
· Pamene pathupi sipanapose masabata 14, othandizira adokotala akhoza chuchotsa pathupipo.
· Dokotala ovomerezeka akhoza kuchotsa pathupi pamasabata aliwonse mogwirizana ndi malamulo.
Uphungu woperekedwa kwa aliyense (Gawo 6)
· Ogwira ntchito zaumoyo ochotsa pathupi akuyenera kupereka uphungu kwa mayi asanamuchotse pathupi komanso atamaliza kumuchotsa pathupi
· Uphungu umenewu ukuyenera kuphatikiza:
o Kusankha pakati posunga kapena kuchotsa pathupi
o Njira zomwe zilipo pochotsa pathupi
o Mavuto anthawi yochepa komaso anthawi yayitali ogwirizana ndi njira iliyonse yochotsera pathupi
o Zotsatira za m’maganizo komanso muubongo zobwera kaamba ka njira iliyonse yochotsera pathupi
o Njira zakulera
Zotsutsa (Gawo 7)
· Pamene munthu sangakwanitse kuchotsa pathupi chifukwa cha zotsutsa zina, munthuyo sazakhala okakamizidwa kugwira ntchito yochotsa pathupi.
· Munthu wokana kuchotsa pathupi chifukwa chazotsutsa zina akuyenera kutumiza mayi wapathupi kwa munthu wina amene ali ndi kuthekera kochotsa pathupi.
o Ngakhale izi zili chonchi, munthu otumiza mayi wapathupi kwa munthu wina akuyenera kufotokozera mayiyu tsatane tsatane wa zimene malamulo akukamba pankhani yochotsa pathupi.
· Ufulu wokana kugwira ntchito yochotsa pathupi ndiwaokhawo omwe akutenga nawo gawo lachindunji pochotsa pathupi.
· Ufulu wokana kugwira ntchito yochotsa pakati sumagwira ntchito ngati kuchotsa pathupiko kuli kofunikira poteteza moyo wa mayi.
Kuti athe kuchotsa pathupi pazifukwa zogwiriridwa komanso mimba yopatsana pachibale, mayi akuyenera kupereka umboni wa mulanduwu (Gawo 8)
· Mayi ofuna kuchotsa pathupi pazifukwa zogwiriridwa kapena pathupi popatsana pachibale akuyenera akhale kuti anakasuma za nkhaniyi ku polisi.
· Pakutero, kuchotsa pathupi kuzachitidwa pokhapokha pamene mayi azatulutsa chikalata cha polisi kupereka kwa ogwira ntchito azaumoyo.
· Kuchotsa pathupi pazifukwa izi kuzaloledwa pokhapokha ngati pathupipo sipanapyole masabata 16.
Chivomerezo (Gawo 9)
· Kuchotsa pathupi kukhoza kuchitika pokhapokha ngati mayi yemwe ali ndi pathupipo wapereka chivomerezo.
· Ngati mayi woyembekezera sangakwanitse kupereka chivomerezo, ogwira ntchito zaumoyo azatenga chilolezochi kwa kholo lovomerezeka ndi malamulo kapena wotsatira wachibale.
· Ngati mwini pathupiyo ali mwana wachichepere, kuchotsa pathupi ndikovomerezedwa pokhapokha ngati pali chilolezo cha kholo lovomerezeka ndi malamulo.
o Ngakhale izi zili chonchi, ngati chivomerezo cha kholo chili chovuta kuperekedwa, ogwira ntchito zaumoyo akhoza kuchotsa pathupi ngati mukuganiza kwake, kopangidwa muchikhulupiriro chabwino, kuchotsa pathupiko ndikwabwino kwa mwanayo.
Chinsinsi (Gawo 10)
· Zambiri komanso zolemba zokhuza kuchotsa pathupi zizasungidwa mwachinsinsi kupatulapo:
o Ngati zizafunidwa ndi munthu ovomerezeka, kuphatikizapo Nduna ya Zaumoyo kapena mkulu wazolembera (registrar).
o Ngati zizafunika pakafukufuku komanso kuti ziwerengeredwe.
o Ngati zizafunika ndi wapolisi ovomerezeka ofufuza ngati pali mulandu ulionse.
o Ngati zizafunika ndi bwalo lamilandu.
o Ngati mayi ochotsa pathupiyo azavomereza kuti ziululidwe kwa munthu wina.
Kayendetsedwe ka madando (Gawo 11)
· Mayi woyembekezera ali ndi ufulu wodandaula ngati wakanizidwa kuchotsa pathupi movomerezeka kapena kupatsidwa chithandizo chili chonse chokhuza izi.
· Chifukwa cha ichi, gawo ili limaika njira yoyendetsera madando ndhicholinga choonetsetsa kuti madando onse aunikidwa komanso chigamulo chaperekedwa.
Milandu ndi zilango zake (Gawo 12 mpaka 16)
· Gawo 12: Munthu yemwe wathandiza mayi kuchotsa pathupi koma siovomeredwa ndi lamulo (kaya ndi wogwira ntchito zaumoyo, mayi wapathupi mwini wake, kapenna munthu wina aliyense) azakhala kundende kwa zaka 14.
· Gawo 13: Munthu aliyense yemwe azagwira ntchito yochotsa pathupi asanapereke uphungu, kapena opanda kulandira chivomerezo, kapena kuphwanya malalamulo osunga chinsinsi azalipira chindapusa cha K3 miliyoni kapena zaka zitatu kundende.
· Gawo 14: Munthu yemwe azapereka chidziwitso chabodza chokhuza kugwirira kapena kugonana pachibale ndi cholinga chofuna kuchotsa pathupi azakhala kundende zaka 5.
· Gawo 15: Munthu yemwe azatchingila mayi kuti athe kuchotsa mimba pamene ali ovomelezedwa ndi malamulo kuti akhoza kutero azapereka chindapusa cha ndalama zokwana K5 miliyoni kapena azakakhala kundende kwa zaka 5.
· Gawo 16: Munthu amene azaphwanya china chilichonse choperekedwa ndi lamuloli koma chilango chake sichinatchulidwe azakhala kundende kwa zaka 5.
Zoperekedwa zosiyanasiyana (Gawo 17 ndi 18)
· Gawo 17 likupereka mphamvu kwa Nduna ya Zaumoyo kuti ikhoza kupanga njira zokhazikitsila lamuloli
· Gawo 18 likuchotsa magawo 149, 150, 151 komanso 243 a mu ndondomeko za malamulo ndi zilango zake